Psalms 137

1Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira
pamene tinakumbukira Ziyoni.
2Kumeneko, pa mitengo ya misondozi
tinapachika apangwe athu,
3pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.
Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;
iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”

4Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova
mʼdziko lachilendo?
5Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,
dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
6Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga
ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,
ngati sindiyesa iwe
chimwemwe changa chachikulu.

7Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita
pa tsiku limene Yerusalemu anagonja.
Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi
mpaka pa maziko ake!”

8Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,
wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera
pa zimene watichitira.
9Amene adzagwira makanda ako
ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.
Copyright information for NyaCCL